Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 1:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. TAONANI Teofilo inu, mau aja oyamba ndinakonza, za zonse Yesu anayamba kuzicita ndi kuziphunzitsa,

2. kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamulira mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha;

3. kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zace, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumuwa Mulungu;

4. ndipo e posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asacoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine;

5. pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.

6. Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa iye, nanena, Ambuye, kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israyeli?

7. Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m'ulamuliro wace wa iye yekha.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 1