Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 9:47-61 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

47. Koma Yesu pakuona kutsutsana kwa mitima yao, anatenga kamwana, nakaimika pambali pace, nati kwa iwo,

48. Amene ali yense akalandire kamwana aka m'dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng'onong'ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkuru.

49. Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikuturutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, cifukwa satsatana nafe.

50. Koma Yesu anati kwa iye, Musamletse, pakuti iye amene satsutsana nanu athandizana nanu.

51. Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe iye kumwamba, Yesu anatsimika kuloza nkhope yace kunka ku Yerusalemu,

52. natumiza amithenga patsogolo pace; ndipo ananka, nalowa m'mudzi wa Asamariya, kukamkonzera iye malo.

53. Ndipo iwo sanamlandira iye, cifukwa nkhope yace inali yoloza kunka ku Yerusalemu.

54. Ndipo pamene ophunzira ace Yakobo ndi Yohane anaona, anati, Ambuye, Kodi mufuna kuti ife tiuze mota utsike kumwamba ndi kuwanyeketsa iwo?

55. Koma iye anapotoloka nawadzudzula.

56. Ndipo anapita kumudzi kwina.

57. Ndipo m'mene iwo analikuyenda m'njira, munthu anati kwa iye, Ine ndidzakutsatani kumene kuli konse mukapitako.

58. Ndipo Yesu anati kwa iye, Nkhandwe ziri nazo nkhwimba, ndi mbalame za kumwamba zisa, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu.

59. Ndipo anati kwa munthu wina, Unditsate Ine. Koma iye anati, Mundilole ine, Ambuye, ndithange ndamuka kuika maliro a atate wanga.

60. Koma anati kwa iye, Leka akufa aike akufa a eni okha; koma muka iwe nubukitse mbiri yace ya Ufumu wa Mulungu.

61. Ndipo winanso anati, Ambuye ndidzakutsatani Inu; koma muthange mwandilola kulawirana nao a kunyumba kwanga.

Werengani mutu wathunthu Luka 9