Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 9:45-56 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

45. Koma iwo sanadziwitse mau awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo anaopa kumfunsa za mau awa.

46. Ndipo anayamba kutsutsana kuti wamkulu mwa iwo ndani.

47. Koma Yesu pakuona kutsutsana kwa mitima yao, anatenga kamwana, nakaimika pambali pace, nati kwa iwo,

48. Amene ali yense akalandire kamwana aka m'dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng'onong'ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkuru.

49. Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikuturutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, cifukwa satsatana nafe.

50. Koma Yesu anati kwa iye, Musamletse, pakuti iye amene satsutsana nanu athandizana nanu.

51. Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe iye kumwamba, Yesu anatsimika kuloza nkhope yace kunka ku Yerusalemu,

52. natumiza amithenga patsogolo pace; ndipo ananka, nalowa m'mudzi wa Asamariya, kukamkonzera iye malo.

53. Ndipo iwo sanamlandira iye, cifukwa nkhope yace inali yoloza kunka ku Yerusalemu.

54. Ndipo pamene ophunzira ace Yakobo ndi Yohane anaona, anati, Ambuye, Kodi mufuna kuti ife tiuze mota utsike kumwamba ndi kuwanyeketsa iwo?

55. Koma iye anapotoloka nawadzudzula.

56. Ndipo anapita kumudzi kwina.

Werengani mutu wathunthu Luka 9