Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 9:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo iye anaitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuciritsa nthenda.

2. Ndipo anawatuma kukalalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuciritsa anthu odwala.

3. Ndipo iye anati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndarama; ndipo musakhale nao malaya awiri.

4. Ndipo m'nyumba iri yonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikacokera kumeneko.

Werengani mutu wathunthu Luka 9