Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 8:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, katapita kamphindi anayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza U thenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndi pamodzi naye khumi ndi awiriwo,

2. ndi akazi ena amene anaciritsidwa mizimu yoipa ndi nthenda zao, ndiwo, Mariya wonenedwa Magadalene, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinaturuka mwa iye,

3. ndi Yohana, mkazi wace wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Susana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi eumacao.

Werengani mutu wathunthu Luka 8