Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 6:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali tsiku la Sabata, iye analinkupita pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ace analinkubudula ngala za tirigu, nazifikisa m'manja mwao, nadya.

2. Koma Afarisi ena anati, Mucitiranji cosaloledwa kucitika tsiku la Sabata?

3. Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi simunawerenganso ngakhale cimene anacita Davine, pamene paja anamva Njala, iye ndi iwo anali naye pamodzi,

4. kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, natenga mikate yoonetsera, nadya, napatsanso iwo anali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe okha?

5. Ndipo iye ananena kwa iwo, kuti, Mwana wa munthu ali Mbuye wa tsiku la Sabata.

6. Ndipo kunali tsiku lina la Sabata, iye analowa m'sunagoge naphunzitsa. Ndipo munali munthu momwemo, ndipo dzanja lace lamanja linali lopuwala.

7. Ndipo alembi ndi Afarisi analikumzonda iye, ngati adzaciritsa tsiku la Sabata; kuti akapeze comneneza iye.

8. Koma iye anadziwa maganizo ao; nati kwa munthuyo wa dzanja lace lopuwala, Nyamuka, nuimirire pakatipo.

9. Ndipo Iyeananyamuka, naimirira. Ndipo Yesuanati kwa iwo, Ndikufunsani inu, Kodi nkulola tsiku la Sabata, kucita zabwino, kapena kucita zoipa? kupulumutsa moyo, kapena kuuononga?

10. Ndipo pamene anaunguza-unguza pa iwo onse, anati kwa iye, Tansa dzanja lako, Ndipo iye anatero, ndi dzanja lace lina; bwerera momwe.

11. Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzace kuti amcitire Yesu ciani.

12. Ndipo kunali masiku awa, iye anaturuka nanka kuphiri kukapemphera; nacezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Luka 6