Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 24:4-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo kunali, m'mene anathedwa nzeru naco, taonani amuna awiri anaimirira pafupi pao atabvala zonyezimira;

5. ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?

6. Palibe kuno iye, komatu anauka; kumbukilani muja adalankhula nanu, pamene analinso m'Galileya,

7. ndi kunena, kuti, Mwana wa munthu ayenera kuperekedwa m'manja a anthu ocimwa, ndi kupacikidwa pamtanda, ndi kuuka tsiku lacitatu.

8. Ndipo anakumbukila mau ace, nabwera kucokera kumanda,

9. nafotokozera zonse khumi ndi mmodziwo, ndi otsala onse omwe.

10. Koma panali Mariya wa Magadala, ndi Y ohana, ndi Mariya amace wa Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nao amene ananena izi kwa atumwiwo.

11. Ndipo mau awa anaoneka pamaso pao ngati nkhani zacabe, ndipo sanamvera akaziwo.

Werengani mutu wathunthu Luka 24