Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 24:27-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za iye yekha.

28. Ndipo anayandikira ku mudzi umene analikupitako; ndipo anacita ngati anafuna kupitirira.

29. Ndipo anamuumiriza iye, nati, Khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu, Ndipo analowa kukhala nao.

30. Ndipo kunali m'mene iye anaseama nao pacakudya, anatenga mkate, naudalitsa naunyema, napatsa iwo.

31. Ndipo maso ao anatseguka, ndipo anamzindikira iye; ndipo anawakanganukira iye, nawacokera.

32. Ndipo anati wina kwa mnzace, Mtima wathu sunali wotentha m'kati mwathu nanga m'mene analankhula nafe m'njira, m'mene anatitseguliramalembo?

33. Ndipo ananyamuka nthawi yomweyo nabwera ku Yerusalemu, napeza khumi ndi mmodziwo, ndi iwo anali nao atasonkhana pamodzi,

34. nanena, Ambuye anauka ndithu, naonekera kwa Simoni.

35. Ndipo iwo anawafotokozera za m'njira, ndi umo anadziwika nao m'kunyema kwa mkate.

Werengani mutu wathunthu Luka 24