Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 24:23-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. ndipo m'mene sanapeza mtembo wace, anadza, nanena kuti adaona m'masomphenya angelo, amene ananena kuti ali ndi moyo iye.

24. Ndipo ena a iwo anali nafe anacoka kunka kumanda, napeza monga momwe akazi adanena; koma Iyeyo sanamuona.

25. Ndipo iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndiozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!

26. Kodi sanayenera Kristu kumva zowawa izi, ndi kulowa ulemerero wace?

27. Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za iye yekha.

28. Ndipo anayandikira ku mudzi umene analikupitako; ndipo anacita ngati anafuna kupitirira.

29. Ndipo anamuumiriza iye, nati, Khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu, Ndipo analowa kukhala nao.

30. Ndipo kunali m'mene iye anaseama nao pacakudya, anatenga mkate, naudalitsa naunyema, napatsa iwo.

Werengani mutu wathunthu Luka 24