Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 24:21-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo tinayembekeza ife kuti iye ndiye wakudzayo kudzaombola Israyeli, Komatunso, pamodzi ndi izi zonse lero ndilo tsiku lacitatu kuyambira zidacitika izi.

22. Komatu akazi enanso a mwa ife anatidabwitsa, ndiwo amene analawirira kumanda;

23. ndipo m'mene sanapeza mtembo wace, anadza, nanena kuti adaona m'masomphenya angelo, amene ananena kuti ali ndi moyo iye.

24. Ndipo ena a iwo anali nafe anacoka kunka kumanda, napeza monga momwe akazi adanena; koma Iyeyo sanamuona.

25. Ndipo iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndiozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!

26. Kodi sanayenera Kristu kumva zowawa izi, ndi kulowa ulemerero wace?

27. Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za iye yekha.

28. Ndipo anayandikira ku mudzi umene analikupitako; ndipo anacita ngati anafuna kupitirira.

29. Ndipo anamuumiriza iye, nati, Khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu, Ndipo analowa kukhala nao.

Werengani mutu wathunthu Luka 24