Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 24:2-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo anapeza mwala unakunkhunizidwa kuucotsa pamanda.

3. Ndipo m'mene analowa sanapeza mtembo wa Ambuye Yesu.

4. Ndipo kunali, m'mene anathedwa nzeru naco, taonani amuna awiri anaimirira pafupi pao atabvala zonyezimira;

5. ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?

6. Palibe kuno iye, komatu anauka; kumbukilani muja adalankhula nanu, pamene analinso m'Galileya,

Werengani mutu wathunthu Luka 24