Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 23:8-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo Herode, pamene anaona Yesu, anakondwa ndithu; pakuti anayamba kale kufuna kumpenya iye, cifukwa anamva za iye; nayembekeza kuona cizindikilo cina cocitidwa ndi iye.

9. Ndipo anamfunsa iye mau ambiri; koma iye sanamyankha kanthu.

10. Ndipo ansembe akuru ndi alembi anaimirira, namnenera iye kolimba.

11. Ndipo Herode ndi asilikari ace anampeputsa iye, namnyoza, nambveka iye copfunda conyezimira, nambwezera kwa Pilato.

12. Ndipo Herode ndi Pilato anaci-I tana cibwenzi tsiku lomwelo; pakuti kale anadana.

13. Ndipo Pilato anaitana ansembe akuru, ndi akuru, ndi anthu, asonkhane,

14. nati kwa iwo, Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo taonani, Ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeza pa munthuyu cifukwa ca zinthu zimene mumnenera;

15. inde, nga khale Herode yemwe; pakuti iye anambwezera iye kwa ife; ndipo taonani, sanacita iye kanthu kakuyenera kufa.

16. Cifukwacace ndidzamkwapula ndi kununasula iye. [

17. ]

18. Koma iwo onse pamodzi anapfuula, nati, Cotsani munthu uyu, mutimasulire Baraba;

19. ndiye munthu anaponyedwa m'ndende cifukwa ca mpanduko m'mudzi ndi ca kupha munthu.

20. Ndipo Pilato analankhulanso nao, nafuna kumasula Yesu;

21. koma iwo anapfuula, nanena, Mpacikeni, mpacikeni pamtanda.

Werengani mutu wathunthu Luka 23