Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 23:50-56 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

50. Ndipo taonani, munthu dzina lace Yosefe, ndiye mkuru wa mirandu, munthu wabwino ndi wolungama

51. (amene sanabvomereza kuweruza kwao ndi nchito yao) wa ku Arimateya, mudzi wa Ayuda, ndiye woyembekezera Ufumu wa Mulungu,

52. yemweyo anapita kwa Pilato napempha mtembo wace wa Yesu.

53. Ndipo 4 anautsitsa, naukulunga m'nsaru yabafuta, nauika m'manda osemedwa m'mwala, m'menemo sanaika munthu ndi kale lonse.

54. Ndipo panali tsiku lokonzera, ndi Sabata linayandikira.

55. Ndipo 5 akazi, amene anacokera naye ku Galileya, anatsata m'mbuyo, naona manda, ndi maikidwe a mtembo wace.

56. Ndipo anapita kwao, 6 nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula 7 monga mwa lamulo.

Werengani mutu wathunthu Luka 23