Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 23:24-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndipo Pilato anaweruza kuti cimene alikufunsa cicitidwe.

25. Ndipo anawamasulira amene adaponyedwa m'ndende cifukwa ca mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo anampempha; koma anapereka Yesu mwa cifuniro cao.

26. Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kurene, alikucokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pace pa Yesu,

27. Ndipo unamtsata unyinji waukuru wa anthu, ndi wa akazi amene anadziguguda pacifuwa, namlirira iye.

28. Koma Yesu anawapotolokera nati, Ana akazi inu a Yerusalemu, musandilirire Ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu.

29. Cifukwa taonani masiku alinkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi mawere osayamwitsa.

30. Pomwepo adzayamba kunena kwa mapiri, Igwani pa ife; ndi kwa zitunda, Bisani ife.

31. Pakuti ngati azicitira izi mtengo wauwisi, nanga kudzatani ndi wouma?

32. Ndipo analinso awiri ena, ndiwo ocita zoipa; anatengedwa pamodzi ndi iye kuti aphedwe.

Werengani mutu wathunthu Luka 23