Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 23:16-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Cifukwacace ndidzamkwapula ndi kununasula iye. [

17. ]

18. Koma iwo onse pamodzi anapfuula, nati, Cotsani munthu uyu, mutimasulire Baraba;

19. ndiye munthu anaponyedwa m'ndende cifukwa ca mpanduko m'mudzi ndi ca kupha munthu.

20. Ndipo Pilato analankhulanso nao, nafuna kumasula Yesu;

21. koma iwo anapfuula, nanena, Mpacikeni, mpacikeni pamtanda.

22. Ndipo anati kwa iwo nthawi yacitatu, Nanga munthuyu anacita coipa ciani? Sindinapeza cifukwa ca kufera iye; cotero ndidzamkwapula iye ndi kummasula.

23. Koma anakakamiza ndi mau okweza, napempha kuti iye apacikidwe, Ndipo mau ao analakika.

24. Ndipo Pilato anaweruza kuti cimene alikufunsa cicitidwe.

25. Ndipo anawamasulira amene adaponyedwa m'ndende cifukwa ca mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo anampempha; koma anapereka Yesu mwa cifuniro cao.

26. Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kurene, alikucokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pace pa Yesu,

27. Ndipo unamtsata unyinji waukuru wa anthu, ndi wa akazi amene anadziguguda pacifuwa, namlirira iye.

28. Koma Yesu anawapotolokera nati, Ana akazi inu a Yerusalemu, musandilirire Ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu.

29. Cifukwa taonani masiku alinkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi mawere osayamwitsa.

Werengani mutu wathunthu Luka 23