Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 22:61-71 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

61. Ndipo Ambuye anapotoloka, nayang'ana Petro. Ndipo 11 Petra anakumbukila mau a Ambuye, kuti anati kwa iye, 12 Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.

62. Ndipo anaturuka, nalira misozi ndi kuwawa mtima.

63. Ndipo amuna amene analikusunga Yesu anamnyoza iye, nampanda.

64. Ndipo anamkulunga iye m'maso, namfunsa, nati, Talota; anakupanda Iwe ndani?

65. Ndipo zambiri zina anamnenera iye, namcitira mwano.

66. Ndipo 13 pamene kunaca, bungwe la akuru a anthu linasonkhana, ndiwo ansembe akuru ndi alembi; ndipo anapita naye ku bwalo lao, nanena, 14 Ngati uli Kristu, utiuze.

67. Ndipo anati kwa iwo, Ndikakuuzani, simudzabvomereza;

68. ndipo ndikakufunsani kanthu, simudzayankha.

69. Koma 15 kuyambira tsopano Mwana wa munthu adzakhala pa dzanja lamanja la mphamvu ya Mulungu.

70. Ndipo onse anati, Umo mtero, muli Mwana wa Mulungu kodi? Ndipo iye anati kwa iwo, 16 Munena kuti ndine.

71. Ndipo iwo anati, 17 Tifuniranjinso mboni? pakuti ife tokha tinamva m'kamwa mwa iye mwini.

Werengani mutu wathunthu Luka 22