Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 22:53-62 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

53. Masiku onse, pamene ndinali ndi inu m'Kacisi, simunatansa manja anu kundigwira: koma 6 nyengo yino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.

54. Ndipo 7 pamenepo anamgwira iye, napita naye, nalowa m'nyumba ya mkulu wa ansembe. Koma Petro anatsata kutari.

55. Ndipo 8 pamene adasonkha mota m'kati mwa bwalo, nakhala pansi pamodzi, Petro anakhala pakati pao.

56. Ndipo mdzakazi anamuona iye alikukhala m'kuwala kwace kwa moto, nampenyetsa iye, nati, Munthu uyunso anali naye.

57. Koma anakana, nati, Mkaziwe, sindimdziwa iye.

58. Ndipo 9 popita kamphindi, anamuona wina, nati, Iwenso uli mmodzi wa awo. Koma Petro anati, Munthu iwe, sindine.

59. Ndipo 10 patapita ngati ora limodzi, wina ananenetsa, kuti, Zoonadi, munthu uyunso anali naye, pakuti ndiye Mgalileya.

60. Koma Petro anati, Munthu iwe, sindidziwa cimene ucinena, Ndipo pomwepo, iye ali cilankhulire, tambala analira.

61. Ndipo Ambuye anapotoloka, nayang'ana Petro. Ndipo 11 Petra anakumbukila mau a Ambuye, kuti anati kwa iye, 12 Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.

62. Ndipo anaturuka, nalira misozi ndi kuwawa mtima.

Werengani mutu wathunthu Luka 22