Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 22:45-58 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

45. Ndipo pamene ananyamuka pakupemphera anadza kwa ophunzira, nawapeza ali m'tulo ndi cisoni,

46. ndipo anati kwa iwo, Mugoneranji? Ukani, 3 pempherani kuti mungalowe m'kuyesedwa.

47. Pamene iye anali cilankhulire, taonani, khamu la anthu, ndipo iye wochedwa Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anawatsogolera; nayandikira Yesu kumpsompsona iye.

48. Koma Yesu anati kwa iye, Yudase, ulikupereka Mwana wa munthu ndi cimpsompsono kodi?

49. Ndipo m'mene iwo akumzinga iye anaona cimene citi cicitike, anati, Ambuye, tidzakantha ndi lupanga kodi?

50. Ndipo wina wa iwo 4 anakantha kapolo wa mkuru wa ansembe, namdula khutu lace lamanja.

51. Koma Yesu anayankha nati, Lolani kufikira kumene. Ndipo anakhudza khutu lace, namciritsa.

52. Ndipo 5 Yesu anati kwa ansembe akulu ndi akapitao a Kacisi, ndi akuru, amene anadza kumgwira iye, Munaturuka ndi malupanga ndi mikunkhu kodi monga ngati kugwira wacifwamba?

53. Masiku onse, pamene ndinali ndi inu m'Kacisi, simunatansa manja anu kundigwira: koma 6 nyengo yino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.

54. Ndipo 7 pamenepo anamgwira iye, napita naye, nalowa m'nyumba ya mkulu wa ansembe. Koma Petro anatsata kutari.

55. Ndipo 8 pamene adasonkha mota m'kati mwa bwalo, nakhala pansi pamodzi, Petro anakhala pakati pao.

56. Ndipo mdzakazi anamuona iye alikukhala m'kuwala kwace kwa moto, nampenyetsa iye, nati, Munthu uyunso anali naye.

57. Koma anakana, nati, Mkaziwe, sindimdziwa iye.

58. Ndipo 9 popita kamphindi, anamuona wina, nati, Iwenso uli mmodzi wa awo. Koma Petro anati, Munthu iwe, sindine.

Werengani mutu wathunthu Luka 22