Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 22:37-51 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

37. Pakuti ndinena ndi inu, cimene cidalembedwa ciyenera kukwanitsidwa mwa Ine, Ndipo anawerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa Ine ziri naco cimariziro.

38. Ndipo iwo anati, Ambuye, taonani, malupanga awir siwa. Ndipo anati kwa iwo, Cakwa nira.

39. Ndipo iye anaturuka, napita monga adafucita, ku phiri la Azitona ndi ophunzira anamtsata iye.

40. Ndipo pofika pomwepo, anati kwa iwo, Pempherani kuti mungalowe m'kuyesedwa.

41. Ndipo anapatukana nao kutalika kwace ngan kuponya mwala, nagwada pansi napemphera,

42. nati, Atate, mukafuna Inu, cotsani cikho ici pa Ine; koma si kufuna kwanga ai, komatu kwanu kucitike.

43. Ndipo anamuonekera iye 1 mngelo wa Kumwamba namlimbitsa iye.

44. Ndipo 2 pokhala iye m'cipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lace linakhala ngati madontho akuru a mwazi alinkugwa pansi.

45. Ndipo pamene ananyamuka pakupemphera anadza kwa ophunzira, nawapeza ali m'tulo ndi cisoni,

46. ndipo anati kwa iwo, Mugoneranji? Ukani, 3 pempherani kuti mungalowe m'kuyesedwa.

47. Pamene iye anali cilankhulire, taonani, khamu la anthu, ndipo iye wochedwa Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anawatsogolera; nayandikira Yesu kumpsompsona iye.

48. Koma Yesu anati kwa iye, Yudase, ulikupereka Mwana wa munthu ndi cimpsompsono kodi?

49. Ndipo m'mene iwo akumzinga iye anaona cimene citi cicitike, anati, Ambuye, tidzakantha ndi lupanga kodi?

50. Ndipo wina wa iwo 4 anakantha kapolo wa mkuru wa ansembe, namdula khutu lace lamanja.

51. Koma Yesu anayankha nati, Lolani kufikira kumene. Ndipo anakhudza khutu lace, namciritsa.

Werengani mutu wathunthu Luka 22