Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 22:26-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkuru mwa inu, akhale ngati wamng'ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira.

27. Pakuti wamkuru ndani, iye wakuseama pacakudya kapena wakutumikirapo? si ndiye wakuseama pacakudya kodi? koma Ine ndiri pakati pa inu monga ngati wotumikira.

28. Koma inu ndinuamene munakhala ndi Ine cikhalire m'mayesero anga;

29. ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu Ufumu wanga;

30. ndipo mudzakhala pa mipando yacifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.

31. Simoni, Simoni, taona, Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu;

32. koma ndinakupempherera kuti cikhulupiriro cako cingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.

33. Ndipo anati kwa iye, Ambuye, ndiripo ndikapite ndi Inu kundende ndikuimfa.

34. Ndipo iye anati, Ndikuuza iwe, Petro, sadzalira tambala lero lino kufikira udzakana katatu kuti sundidziwa Ine.

35. Ndipo anati kwa iwo, Pamene ndinakutumizani opanda thumba la ndalama, ndi thumba la kamba, ndi nsapato, munasowa kanthu kodi? Anati iwo, Iai.

36. Ndipo anati kwaiwo, Koma tsopano, iye amene ali ndi thumba la ndalama, alitenge, ndi thumba la kamba lomwe; ndipo amene alibe, agulitse copfunda cace, nagule lupanga,

37. Pakuti ndinena ndi inu, cimene cidalembedwa ciyenera kukwanitsidwa mwa Ine, Ndipo anawerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa Ine ziri naco cimariziro.

Werengani mutu wathunthu Luka 22