Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 22:22-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Pakuti Mwana wa munthu amukatu, monga kunaikidwiratu; koma tsoka munthuyo amene ampereka!

23. Ndipo anayamba kufunsana mwa iwo okha, ndiye yani mwa iwo amene adzacita ici.

24. Ndipo kunakhala kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkuru.

25. Ndipo anati kwa iwo, Mafumu a anthu a mitundu awacitira ufumu; ndipo iwo amene awacitira ulamuliro anenedwa, Ocitira zabwino.

26. Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkuru mwa inu, akhale ngati wamng'ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira.

27. Pakuti wamkuru ndani, iye wakuseama pacakudya kapena wakutumikirapo? si ndiye wakuseama pacakudya kodi? koma Ine ndiri pakati pa inu monga ngati wotumikira.

28. Koma inu ndinuamene munakhala ndi Ine cikhalire m'mayesero anga;

29. ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu Ufumu wanga;

30. ndipo mudzakhala pa mipando yacifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.

31. Simoni, Simoni, taona, Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu;

32. koma ndinakupempherera kuti cikhulupiriro cako cingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.

33. Ndipo anati kwa iye, Ambuye, ndiripo ndikapite ndi Inu kundende ndikuimfa.

Werengani mutu wathunthu Luka 22