Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 22:10-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo iye anati kwa iwo, Onani, mutalowa m'mudzi, adzakomana ndinu munthu alikusenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akalowako iye.

11. Ndipo mukanene kwa mwini nyumbayo, Mphunzitsi anena nawe, Cipinda ca alendo ciri kuti, m'mene ndikadye Paskha pamodzi ndi ophunzira anga?

12. Ndipo iyeyo adzakuonetsani cipinda cacikuru capamwamba, cokonzeka; mukakonzere kumeneko.

13. Ndipo anapita iwo, napeza monga adatero nao; ndipo anakonza Paskha.

14. Ndipo itadza nthawi yace, iye anakhala pacakudya, ndi ophunzira pamodzi ndi iye.

15. Ndipo anati kwa iwo, Ndinalakalaka ndithu kudya Paskha uwu pamodzi ndinu, ndisanayambe kusautsidwa;

16. pakuti ndinena ndi inu, sindidzadya kufikira udzakwaniridwa mu Ufumu wa Mulungu.

17. Ndipo analandira cikho, ndipo pamene adayamika, anati, Landirani ici, mucigawane mwa inu nokha;

18. pakuti ndinena kwa inu, kuyambira tsopano Ine sindidzamwako cipatso ca mpesa, kufikira Ufumu wa Mulungu udzafika.

19. Ndipo m'mene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, ici ndi thupi langa lopatsidwa cifukwa ca inu; citani ici cikumbukilo canga.

20. Ndipo coteronso cikho, atatha mgonero, nanena, Cikho ici ndi pangano latsopano m'mwazi wanga wothiridwa cifukwa ca inu.

21. Koma onani, dzanja lace la iye amene adzandipereka ali pagome pano pamodzi ndi Ine.

22. Pakuti Mwana wa munthu amukatu, monga kunaikidwiratu; koma tsoka munthuyo amene ampereka!

23. Ndipo anayamba kufunsana mwa iwo okha, ndiye yani mwa iwo amene adzacita ici.

24. Ndipo kunakhala kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkuru.

25. Ndipo anati kwa iwo, Mafumu a anthu a mitundu awacitira ufumu; ndipo iwo amene awacitira ulamuliro anenedwa, Ocitira zabwino.

26. Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkuru mwa inu, akhale ngati wamng'ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira.

Werengani mutu wathunthu Luka 22