Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 22:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo phwando la mikate yopanda cotupitsa linayandikira, ndilo lochedwa Paskha.

2. Ndipo ansembe akuru ndi alembi anafunafuna maphedwe ace pakuti anaopa anthuwoo.

3. Ndipo Satana analowa m'Yudase wonenedwa Isikariote, amene anawerengedwa mmodzi wa khumi ndi awiriwo,

4. Ndipo iye anacoka, nalankhulana ndi ansembe akulu ndi akazembe mompereka iye kwa iwo.

5. Ndipo anakondwera, napangana naye kumpatsa ndalama.

6. Ndipo iye anabvomera, nafunafuna nthawi yabwino yakumpereka iye kwa iwo, pakalibe khamu la anthu.

7. Ndipo tsiku la mikate yopanda cotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paskha.

8. Ndipo iye anatumiza Petro ndi Yohane, nati, Pitanimutikonzere ife Paskha, kuti tidye.

9. Ndipo iwo ananena naye, Mufuna tikakonzere kuti?

10. Ndipo iye anati kwa iwo, Onani, mutalowa m'mudzi, adzakomana ndinu munthu alikusenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akalowako iye.

Werengani mutu wathunthu Luka 22