Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 21:26-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekeeera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi;

27. pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa munthu alinkudza mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukuru.

28. Komapoyamba kucitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; cifukwa ciomboledwe canu cayandikira.

29. Ndipo ananena nao fanizo; Onani mkuyu, ndi mitengo yonse:

30. pamene iphukira, muipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja liri pafupi pomwepo.

31. Inde cotero inunso, pakuona zinthu izi zirikucitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.

32. Indetu ndinena ndinu, Mbadwo uno sudzapitirira, kufikira zonse zitacitika.

33. Kumwamba ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.

34. Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;

35. pakuti Iidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi.

36. Koma inu dikirani nyengo zonse ndi kupemphera, kutimukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzacitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.

37. Ndipo usana uli wonse iye analikuphunzitsa m'Kacisi; ndi usiku uli wonse anaturuka, nagona pa phiri lochedwa la Azitona.

38. Ndipo anthu onse analawira mamawa kudza kwa iye kuKacisi kudzamvera Iye.

Werengani mutu wathunthu Luka 21