Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 21:25-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo kudzakhala zizindikilo pa dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi pa dziko lapansi cisauko ca mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkukumo wace wa nyanja ndi mafunde ace;

26. anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekeeera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi;

27. pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa munthu alinkudza mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukuru.

28. Komapoyamba kucitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; cifukwa ciomboledwe canu cayandikira.

29. Ndipo ananena nao fanizo; Onani mkuyu, ndi mitengo yonse:

30. pamene iphukira, muipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja liri pafupi pomwepo.

31. Inde cotero inunso, pakuona zinthu izi zirikucitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.

32. Indetu ndinena ndinu, Mbadwo uno sudzapitirira, kufikira zonse zitacitika.

33. Kumwamba ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.

34. Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;

Werengani mutu wathunthu Luka 21