Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 21:22-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Cifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zicitike.

23. Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi iwo akuyamwitsa ana masiku awo! pakuti padzakhala cisauko cacikuru padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa.

24. Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka ku mitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.

25. Ndipo kudzakhala zizindikilo pa dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi pa dziko lapansi cisauko ca mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkukumo wace wa nyanja ndi mafunde ace;

26. anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekeeera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi;

27. pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa munthu alinkudza mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukuru.

28. Komapoyamba kucitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; cifukwa ciomboledwe canu cayandikira.

Werengani mutu wathunthu Luka 21