Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 20:40-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

40. Pakuti sanalimbanso mtima kumfunsa iye kanthu kena.

41. Koma iye anati kwa iwo, Amanena bwanji kuti Kristuyo ndiye mwana wa Davine?

42. Pakuti Davine yekha anena m'buku la Masalmo,Ambuye ananena kwa Ambuye wanga,Ukhale pa dzanja langa lamanja,

43. Kufikira Ine ndikaika adani akopansi pa mapazi ako.

44. Cotero Davine anamchula iye Ambuye, ndipo nanga ali mwana wace bwanji?

45. Ndipo pamene anthu onse anallinkumva iye, anati kwa ophunzira,

46. Cenjerani nao alembi, amene afuna kuyendayenda obvala miinjiro, nakonda kulankhulidwa m'misika, ndi mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamapwando;

47. amene aononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga acita mai pemphero atali; amenewo adzalandira kulanga koposa.

Werengani mutu wathunthu Luka 20