Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 20:28-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. nanena, Mphunzitsi, Mose anatilembera ire, kuti mbale wace wa munthu akafa, wokhala ndi mkazi, ndipo ali be mwana iye, mbale wace adzakwatira mkaziyo, nadzamuukitsira mbale wace mbeu.

29. Tsono panali abale asanu ndi awiri; ndipo woyamba anakwatira mkazi, nafa wopanda mwana;

30. ndipo waciwiri,

31. ndi wacitatu anamtenga mkaziyo; ndipo coteronso asanu ndi awiri onse, sanasiya mwana, namwalira.

32. Pomarizira anamwaliranso mkaziyo.

33. Potero m'kuuka iye adzakhala mkazi wa yani wa iwo? pakuti asanu ndi awiriwo adamkwatira iye.

34. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ana a dziko lapansi akwatira nakwatiwa:

35. koma iwo akuyesedwa oyenera kufikira dzikolijalo, ndi kuuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa.

36. Pakuti sangathe kufanso nthawi zonse; pakuti afanafana ndi angelo; ndipo ali ana a Mulungu, popeza akhala ana a kuuka kwa akufa.

37. Koma za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Citsamba cija, pamene iye amchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.

38. Ndipo iye sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa iye.

39. Ndipo alembi ena anayankha nati, Mphunzitsi, mwanena bwino.

Werengani mutu wathunthu Luka 20