Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 20:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali lina la masiku awo m'mene iye analikuphunzitsa anthu m'Kacisi, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, adamdzera ansembe akulu ndi alembi pamodzi ndi akulu;

2. ndipo anati, nanena naye, Mutiuze mucita in ndi ulamuliro wotani? Kapena ndani iye amene anakupatsani ulamuliro umene?

3. Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Ndidzakufunsani mau Inenso; mundiuze:

4. Ubatizo wa Yohane unacokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu?

5. Ndipo anatsutsana mwa okha, nanena, Ngati tinena ucokera Kumwamba; adzati, Simunamkhulupirira cifukwa ninji?

6. ndiponso, tikanena, Ucokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri.

7. Ndipo anayankha kuti sadziwa kumene ucokera.

8. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndingakhale Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndicita nao zinthu izi.

9. Ndipo iye anayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu analima munda wamphesa, naukongoletsa kwa olima munda, nanka ku dziko lina, nagonerako nthawi yaikuru.

10. Ndipo pa nyengo ya zipatso anatumiza kapolo wace kwa olima mundawo, kuti ampatseko cipatso ca mundawo; koma olimawo anampanda, nambweza wopanda kanthu.

11. Ndipo anatumizanso kapolo wina; ndipo iyenso anampanda, namcitira cipongwe, nambweza, wopanda kanthu.

12. Ndipo anatumizanso wina wacitatu; ndipo iyenso anamlasa, namtaya kunja.

Werengani mutu wathunthu Luka 20