Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 2:32-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Kuunika kukhale cibvumbulutso ca kwa anthu a mitundu,Ndi ulemerero wa anthu anu Israyeli.

33. Ndipo atate ndi amace anali kuzizwa ndi zinthu zolankhulidwa za iye.

34. Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Mariya amace, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa. Israyeli; ndipo akhale cizindikilo cakutsutsana naco;

35. eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako; kuti maganizo a m'mitima yambiri akaululidwe.

36. Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanueli, wa pfuko la Aseri; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wace, kuyambira pa unamwali wace,

37. zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zace: makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sanacoka kuKacisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.

38. Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, nabvomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za iye kwa anthu onse 1 akuyembekeza ciombolo ca Yerusalemu.

39. Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa cilamulo ca Ambuye, anabwera ku Galileya, ku mudzi kwao, ku Nazarete.

40. Ndipo 2 mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi cisomo ca Mulungu cinali pa iye.

41. Ndipo atate wace ndi amace 3 akamuka caka ndi caka ku Yerusalemu ku Paskha.

Werengani mutu wathunthu Luka 2