Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 2:12-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo ici ndi cizindikilo kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsaru atagonamodyera.

13. Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena,

14. Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba,Ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.

15. Ndipo panali, pamene angelo anacokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzace, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone cinthu ici cidacitika, cimene Ambuye anatidziwitsira ife.

16. Ndipo iwo anadza ndi cangu, napeza Mariya, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera.

17. Ndipo iwo, m'mene anaona, anadziwitsa anthu za mau analankhulidwa kwa iwo a mwana uyu.

18. Ndipo anthu onse amene anamva anazizwa ndi zinthu abusa adalankhula nao.

19. Koma Mariya anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwace.

20. Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo.

21. Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula iye, anamucha dzina lace Yesu, limene anachula mngeloyo asanalandiridwe iye m'mimba.

22. Ndipo pamene anakwanira masiku a kukonza kwao, monga mwa cilamulo ca Mose, iwo anakwera naye kunka ku Yerusalemu, kukamsonyeza iye kwa Ambuye,

23. (monga mwalembedwa m'cilamulo ca Ambuye, kuti mwamuna ali yense wotsegula pa mimba ya amace adzanenedwa wopatulika wa kwa Ambuye)

24. ndi kukapereka nsembe monga mwanenedwa m'citamulo ca Ambuye, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri.

25. Ndipo onani, m'Yerusalemu munali munthu, dzina lace Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israyeli; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.

26. Ndipo anamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaona Kristu wace wa Ambuye.

27. Ndipo iye analowa kuKacisi ndi Mzimu: ndipo pamene atate ndi amace analowa ndi kamwanako Yesu, kudzamcitira iye mwambo wa cilamulo,

28. pomwepo iye anamlandira iye m'manja mwace, nalemekeza Mulungu, nati,

29. Tsopano, Ambuye, monga mwa mau anu aja,Lolani ine, kapolo wanu, ndicoke mumtendere;

Werengani mutu wathunthu Luka 2