Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 19:36-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Ndipo pakupita iye, anayala zobvala zao m'njira.

37. Ndipo pakuyandikira iye tsono potsetsereka pace pa phiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau akuru, cifukwa ca nchito zonse zamphamvu anaziona;

38. nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m'dzina la Ambuye; mtendere m'Mwamba, ndi ulemerero m'Mwambamwamba.

39. Ndipo Afarisi ena a m'khamu la anthu anati kwa iye, Mphunzitsi, dzudzulani ophunzira anu.

40. Ndipo anayankha nati, Ndinena ndi inu, ngati awa akhala cete miyala idzapfuula.

41. Ndipo m'meneanayandikira, anaona mudziwo naulirira,

42. nanena, Ukadazindikira tsiku ili, inde iwetu zinthu za mtendere! koma tsopano zibisika pamaso pako.

43. Pakuti masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo;

44. ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa mwala unzace; popeza sunazindikira nyengo, ya mayang'aniridwe ako.

45. Ndipo analowa m'Kacisi, nayamba kuturutsa iwo akugulitsa malonda, nanena nao,

46. Kwalembedwa, Ndipo nyumba yanga idzakhala nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa iyo phanga la acifwamba.

47. Ndipo analikuphunzitsa m'Kacisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe akulu, ndi alembi ndi akulu a anthu anafunafuna kumuononga iye;

Werengani mutu wathunthu Luka 19