Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 19:23-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. ndipo sunapereka bwanji ndalama yanga pokongoletsa, ndipo ine pakudza ndikadaitenga ndi phindu lace?

24. Ndipo anati kwa iwo akuimirirapo, Mcotsereni ndalamayo, nimuipatse kwa iye wakukhala nazo ndalama khumi.

25. Ndipo anati kwa iye, Mbuye, ali nazo ndalama khumi.

26. Ndinena ndi inu, kuti kwa yense wakukhala naco kudzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe kanthu, cingakhale cimene ali naco cidzacotsedwa.

27. Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani cao kuno, nimuwaphe pamaso panga,

28. Ndipo m'mene adanena izi anawatsogolera nakwera ku Yerusalemu.

29. Ndipo kunali, m'mene anayandikira ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri lochedwa la Azitona, anatuma awiri a ophunzira,

30. nati, Mukani ku mudzi uli pandunji panu; m'menemo, polowa, mudzapeza mwana wa buru womangidwa, pamenepo palibe munthu anakwerapo nthawi iri yonse; mummasule iye nimumtenge.

31. Ndipomunthuakati kwa inu, Mummasuliranji? mudzatero naye, Ambuye amfuna iye.

32. Ndipo anacoka otumidwawo, napeza monga adanena kwa iwo.

33. Ndipo pamene anamasula mwana wa buru, eni ace anati kwa iwo, Mumasuliranji mwana wa buru?

34. Ndipo anati, Ambuye amfuna iye.

35. Ndipo anadzanave kwa Yesu; ndipo anayalika zobvala zao pa mwana wa buruyo, nakwezapo Yesu.

36. Ndipo pakupita iye, anayala zobvala zao m'njira.

37. Ndipo pakuyandikira iye tsono potsetsereka pace pa phiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau akuru, cifukwa ca nchito zonse zamphamvu anaziona;

Werengani mutu wathunthu Luka 19