Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 18:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafoka mtima;

2. nanena, M'mudzi mwakuti munali woweruza wosaopa Mulungu, ndi wosasamala munthu.

3. Ndipo m'mudzimo munali mkazi wamasiye; ndipo anadza kwa iye nanena, Mundiweruzire mlandu pa wotsutsana nane.

4. Ndipo sanafuna nthawi; koma bwino bwino anati mwa yekha, Ndingakhale sindiopa Mulungu kapena kusamala munthu;

5. koma cifukwa ca kundibvuta ine mkazi wamasiye amene ndidzamweruzira mlandu, kuti angandilemetse ndi kudzaidza kwace.

6. Ndipo Ambuye anati, Tamverani conena woweruza wosalungama.

7. Ndipo kodi Mulungu sadzacitira cilungamo osankhidwa ace akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?

Werengani mutu wathunthu Luka 18