Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 17:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Kadzicenjerani nokha; akacimwa mbale wako umdzudzule; akalapa, umkhululukire.

4. Ndipo akakucimwira kasanu ndi kawiri pa tsiku lace, nakakutembenukira kasanu ndi kawiri ndi kunena, Ndalapa ine; uzimkhululukira.

5. Ndipo atumwi anati kwa Ambuye, Mutionjezere cikhulupiriro.

6. Koma Ambuye anati, Mukakhala naco cikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu.

7. Koma ndani mwa inu ali naye kapolo wolima, kapena woweta nkhosa, amene pobwera iye kucokera kumunda adzanena kwa iye, Lowa tsopano, khala pansi kudya;

8. wosanena naye makamaka, Undikonzere cakudya me, nudzimangire, nunditumikire kufikira ndadya ndi kumwa; ndipo nditatha ine udzadya nudzamwa iwe?

9. Kodi ayamika kapoloyocifukwa anacita zolamulidwa?

Werengani mutu wathunthu Luka 17