Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 17:11-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo kunali, pakumuka ku Yerusalemu iye analikupita pakati pa Samariya ndi Galileya.

12. Ndipo m'mene analowa iye m'mudzi wina, anakomana naye amuna khumi akhate, amene anaima kutali;

13. ndipo iwo anakweza mau, nanena, Yesu, Mbuye, muticitire cifundo.

14. Ndipo pakuwaona anati kwa iwo, Pitani, kadzionetseni nokha kwa ansembe. Ndipo kunali, m'kumuka kwao, anakonzedwa.

15. Ndipo mmodzi wa iwo, pakuona kuti anaciritsidwa, anabwerera m'mbuyo, nalemekeza Mulungu ndi mau akuru;

16. ndipo anagwa nkhope yace pansi ku mapazi ace, namyamika iye; ndipo anali Msamariya ameneyo.

17. Ndipo Yesu anayankha nati, Kodi sanakonzedwa khumi? koma ali kuti asanu ndi anai aja?

18. Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeka mmodzi kodi, koma mlendo uyu?

19. Ndipo anati kwa iye, Nyamuka, nupite; cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe.

20. Ndipo pamene Afarisi anamfunsa iye, kuti, Ufumu wa Mulungu ukudza liti, anawayarikha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe;

21. ndipo sadzanena, Taonani uwu, kapena uwo! Pakuti, taonani, Ufumu wa Mulungu uli m'kati mwa inu.

22. Ndipo anati kwa ophunzira ace, Adzadza masiku, amene mudzakhumba kuona limodzi la masiku a Mwana wa munthu, koma simudzaliona.

Werengani mutu wathunthu Luka 17