Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 17:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anati kwa ophunzira ace, Sikutheka kuti zolakwitsa zisadze; koma tsoka iye amene adza nazo.

2. Kukolowekedwa mwala wamphero m'khosi mwace ndi kuponyedwa Iye m'nyanja nkwapafupi, koma kulakwitsa mmodzi wa ang'ono awa nkwapatali.

3. Kadzicenjerani nokha; akacimwa mbale wako umdzudzule; akalapa, umkhululukire.

4. Ndipo akakucimwira kasanu ndi kawiri pa tsiku lace, nakakutembenukira kasanu ndi kawiri ndi kunena, Ndalapa ine; uzimkhululukira.

5. Ndipo atumwi anati kwa Ambuye, Mutionjezere cikhulupiriro.

6. Koma Ambuye anati, Mukakhala naco cikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu.

7. Koma ndani mwa inu ali naye kapolo wolima, kapena woweta nkhosa, amene pobwera iye kucokera kumunda adzanena kwa iye, Lowa tsopano, khala pansi kudya;

8. wosanena naye makamaka, Undikonzere cakudya me, nudzimangire, nunditumikire kufikira ndadya ndi kumwa; ndipo nditatha ine udzadya nudzamwa iwe?

9. Kodi ayamika kapoloyocifukwa anacita zolamulidwa?

10. Cotero Inunso m'mene mutacita zonse anakulamulirani, Denani, Ife ndife akapolo opanda pace, tangocita zimene tayenera kuzicita.

11. Ndipo kunali, pakumuka ku Yerusalemu iye analikupita pakati pa Samariya ndi Galileya.

12. Ndipo m'mene analowa iye m'mudzi wina, anakomana naye amuna khumi akhate, amene anaima kutali;

Werengani mutu wathunthu Luka 17