Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 16:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo iye ananenanso kwa ophunzira ace, Panali munthu mwini cuma, anali ndi kapitao wace; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza cuma cace.

2. Ndipo anamuitana, nati kwa iye, ici ndi ciani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao.

3. Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwace, Ndidzacita ciani, cifukwa mbuye wanga andicotsera ukapitao? kulima ndiribe mphamvu, kupemphapempha kundicititsa manyazi.

4. Ndidziwa cimene ndidzacita, kotero kuti pamene ananditurutsa muukapitao, anthu akandilandire kunyumba kwao.

5. Ndipo anadziitanira mmodzi ndi mmodzi amangawa onse a mbuye wace, nanena kwa woyamba, Unakongola ciani kwa mbuye wanga?

6. Ndipo anati, Mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye ananena naye, Tenga kalata wako, nukhale pansi msanga, nulembere, Makumi asanu.

7. Pomwepo anati kwa wina, Ndipo iwe uli nao mangawa otani? Ndipo uyu anati, Mitanga ya tirigu zana iye ananena naye, Tenga kalata wako nulembere makumi asanu ndi atatu.

Werengani mutu wathunthu Luka 16