Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 15:23-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. ndipo idzani naye mwana wa ng'ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere;

24. cifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa. Ndipo anayamba kusekera.

25. Koma mwana wace wamkuru anali kumunda. Ndipo pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba, anamva kuyimba ndi kubvina.

26. Ndipo anaitana mmodzi wa anayamata, namfunsa, Zinthu izi nzotani?

27. Ndipo uyu anati kwa iye, Mng'ono wako wafika; ndipo atate wako anapha mwana wa ng'ombe wonenepa, cifukwa anamlandira iye wamoyo.

28. Koma anakwiya, ndipo sanafuna kulowamo, Ndipo atate wace anaturuka namdandaulira.

29. Koma anayankha nati kwa atate wace, Onani, ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindinalakwira lamulo lanu nthawi iri yonse; ndipo simunandipatsa ine kamodzi konse mwana wa mbuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga.

30. Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha zamoyo zanu ndi akazi aciwerewere, munamphera iye mwana wa ng'ombe wonenepa.

31. Koma iye ananena nave, Mwana wanga, iwe uli ndine nthawi zonse, ndipo zanga zonse ziri zako.

32. Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: cifukwa mng'ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.

Werengani mutu wathunthu Luka 15