Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 14:30-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumariza.

31. Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu inzace, sathanga wakhala pansi, nafunsana ndi akuru ngati akhoza ndi asilikari ace zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikari zikwi makumi awiri?

32. Koma ngati sakhoza, atumiza akazembe, pokhala winayo ali kutalitali, nafunsa za mtendere.

33. Cifukwa cace tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sakhoza kukhala wophunzira wanga.

34. Kotero mcere uli wokoma; koma ngati mcere utasukuluka adzaukoleretsa ndi ciani?

35. Suyenera kuuthira pamunda kapena padzala, autaya kunja. Amene ali nao makutu akumva amve.

Werengani mutu wathunthu Luka 14