Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 14:19-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo anati wina, Ine ndagula ng'ombe za magori asanu, ndipo ndinka kukaziyesa; ndikupempha undilole ine ndisafika.

20. Ndipo anati wina, Ine ndakwatira mkazi, ndipo cifukwa cace sindingathe kudza.

21. Ndipo kapoloyo pakubwera anauza mbuye wace zinthu izi. Pamenepo mwini nyumba anakwiya, nati kwa kapolo wace, Turuka msanga, pita kumakwalala ndi ku njira za mudzi, nubwere nao muno aumphawi ndi opunduka ndi akhungu ndi otsimphina.

22. Ndipo kapoloyo anati, Ambuye, cimene munacilamulira cacitika, ndipo malo atsalapo.

23. Ndipo mbuye ananena kwa kapoloyo, Turuka, nupite kumiseu ndi njira za kuminda, nuwaumirize anthu alowe, kuti nyumba yanga idzale.

24. Pakuti ndinena kwa inu, kuti kulibe mmodzi wa amuna oitanidwa aja adzalawa phwando langa.

25. Ndipo mipingo yambiri ya anthu inamuka naye; ndipo iye anapotoloka, nati kwa iwo.

Werengani mutu wathunthu Luka 14