Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 12:19-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli naco cuma cambiri cosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.

20. Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?

21. Atero iye wakudziunjikira cuma mwini yekha wosakhala naco cuma ca kwa Mulungu,

22. Ndipo Iyeanati kwa ophunzira ace, Cifukwa cace ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, cimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, cimene mudzabvala.

23. Pakuti moyo uli woposa cakudya, ndi thupi liposa cobvala.

24. Lingirirani makungubwi, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa: nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!

25. Ndipo ndani wa inu, ndi kuda nkhawa angathe kuonjeza mkono pa msinkhu wace?

26. Kotero ngati simungathe ngakhale cacing'onong'ono, muderanji nkhawa cifukwa ca zina zija?

27. Lingalirani maluwa, makulidwe ao; sagwiritsa nchito ndi kusapota; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomo, mu ulemerero wace wonse, sanabvala ngati limodzi la awa.

Werengani mutu wathunthu Luka 12