Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 12:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena.

13. Ndipo munthu wa m'khamulo anati kwa iye, Mphunzitsi, uzani mbale wanga agawane ndi ine cuma camasiye.

14. Koma anati kwa iye, Munthu iwe, ndani anandiika Ine ndikhale woweruza, kapena wakugawira inu?

15. Ndipo iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uli wonse; cifukwa moyo wace wa munthu sulingana ndi kucuruka kwa zinthu zace ali nazo.

16. Ndipo iye ananena nao fanizo, kuti, Munda wace wa munthu mwini cuma unapatsa bwino.

17. Ndipo anaganizaganiza mwa yekha nanena, Ndidzatani ine, popeza ndiribe mosungiramo zipatso zanga?

18. Ndipo anati, Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikuru, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi cuma canga.

19. Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli naco cuma cambiri cosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.

Werengani mutu wathunthu Luka 12