Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 12:10-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo amene ali yense adzanenera Mwana wa munthu zoipa adzakhululukidwa; koma amene anenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa.

11. Ndipo pamene pali ponse adzamuka nanu ku mlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena ciani;

12. pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena.

13. Ndipo munthu wa m'khamulo anati kwa iye, Mphunzitsi, uzani mbale wanga agawane ndi ine cuma camasiye.

14. Koma anati kwa iye, Munthu iwe, ndani anandiika Ine ndikhale woweruza, kapena wakugawira inu?

15. Ndipo iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uli wonse; cifukwa moyo wace wa munthu sulingana ndi kucuruka kwa zinthu zace ali nazo.

16. Ndipo iye ananena nao fanizo, kuti, Munda wace wa munthu mwini cuma unapatsa bwino.

17. Ndipo anaganizaganiza mwa yekha nanena, Ndidzatani ine, popeza ndiribe mosungiramo zipatso zanga?

18. Ndipo anati, Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikuru, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi cuma canga.

19. Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli naco cuma cambiri cosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.

20. Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?

21. Atero iye wakudziunjikira cuma mwini yekha wosakhala naco cuma ca kwa Mulungu,

22. Ndipo Iyeanati kwa ophunzira ace, Cifukwa cace ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, cimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, cimene mudzabvala.

Werengani mutu wathunthu Luka 12