Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 12:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pomwepo pamene anthu a zikwi zikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, iye anayamba kunena kwa ophunzira ace poyamba, Tacenierani nokha ndi cotupitsa mikate ca Afarisi, cimeneciri cinyengo.

2. Koma kulibe kanthu kobvundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika.

3. Cifukwa cace zonse zimene mwazinena mumdima zidzamveka poyera; ndipo cimene mwalankhula m'khutu, m'zipinda za m'kati cidzalalikidwa pa macindwi a nyumba.

4. Ndipo ndinena kwa inu, abwenzi anga, Musaope iwo akupha thupi, ndipo akatha ici alibe kanthu kena angathe kucita.

5. Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya kugehena, inde, ndinena ndinu opani ameneyo.

6. Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu;

7. komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wace wa mpheta zambiri.

8. Ndipo ndinena kwa inu, Amene ali yense akabvomereza Ine pamaso pa anthu, inde, Mwana wa munthu adzambvomereza iye pamaso pa angelo a Mulungu;

Werengani mutu wathunthu Luka 12