1. Pomwepo pamene anthu a zikwi zikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, iye anayamba kunena kwa ophunzira ace poyamba, Tacenierani nokha ndi cotupitsa mikate ca Afarisi, cimeneciri cinyengo.
2. Koma kulibe kanthu kobvundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika.
3. Cifukwa cace zonse zimene mwazinena mumdima zidzamveka poyera; ndipo cimene mwalankhula m'khutu, m'zipinda za m'kati cidzalalikidwa pa macindwi a nyumba.
4. Ndipo ndinena kwa inu, abwenzi anga, Musaope iwo akupha thupi, ndipo akatha ici alibe kanthu kena angathe kucita.