Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 11:50-54 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

50. kuti mwazi wa aneneri onse, wakhetsedwa kuyambira kukhazika kwa dziko lapansi, ukafunidwe kwa anthu a mbadwo uno;

51. kuyambira mwazi wa 1 Abele kufikira mwazi wa 2 Zakariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kacisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.

52. 3 Tsoka inu, acilamulo! cifukwa munacotsa cifungulo ca nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa.

53. Ndipo pamene iye anaturuka m'menemo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza iye kolimba, ndi kumtompha iye ndi zinthu zambiri;

54. 4 namlindira akakole kanthu koturuka m'kamwa mwace.

Werengani mutu wathunthu Luka 11