Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 11:48-53 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

48. Comweco muli mboni, ndipo mubvomera nchito za makolo anu; cifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda.

49. Mwa icinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;

50. kuti mwazi wa aneneri onse, wakhetsedwa kuyambira kukhazika kwa dziko lapansi, ukafunidwe kwa anthu a mbadwo uno;

51. kuyambira mwazi wa 1 Abele kufikira mwazi wa 2 Zakariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kacisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.

52. 3 Tsoka inu, acilamulo! cifukwa munacotsa cifungulo ca nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa.

53. Ndipo pamene iye anaturuka m'menemo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza iye kolimba, ndi kumtompha iye ndi zinthu zambiri;

Werengani mutu wathunthu Luka 11