Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 10:38-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Ndipo pakupita paulendo pao iye analowa m'mudzi wina; ndipo mkazi wina dzina lace 4 Marita anamlandira iye kunyumba kwace.

39. Ndipo anali ndi mbale wace wochedwa Mariya, ndiye wakukhala pa mapazi a Ambuye, namva mau ace.

40. Koma Marita anatekeseka ndi kutumikira kwambiri; ndipo anadzako nati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze tsono kuti andithandize.

41. Koma Ambuye anayankha nati kwa iye, Marita, Marita, uda nkhawa nubvutika ndi zinthu zambiri;

42. koma cisoweka cinthu cimodzi, pakuti Mariya anasankha dera lokoma limene lsilidzacotsedwa kwa iye.

Werengani mutu wathunthu Luka 10