Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 10:25-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo taonani, wacilamulo wina anaimirira namuyesa iye, nanena, 2 Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kucita ciani?

26. Ndipo anati kwa iye, M'cilamulo mulembedwa ciani? Uwerenga bwanji?

27. Ndipo iye anayankha nati, 3 Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.

28. Ndipo anati kwa iye, Wayankha bwino; cita ici, ndipo udzakhala ndi moyo.

29. Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani?

30. Ndipo Yesu anamlanda mau, nati, Munthu wina anatsika kucokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m'manja a acifwamba amene anambvula zobvala, namkwapula, nacoka atamsiya wofuna kufa.

31. Ndipo kudangotero kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuona iye anapita mbali yina.

32. Momwemonso Mlevi, pofika pamenepo, ndi kumuona, anapita mbali yina.

33. Koma Msamariya wina ali pa ulendo wace anadzapali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa cifundo,

34. nadza kwa iye, namanga mabala ace, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yace ya iye yekha, nadza naye ku nyumba ya alendo, namsungira.

35. Ndipo m'mawa mwace anaturutsa marupiya atheka awiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Msungire iye, ndipo ciri conse umpatsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe.

36. Uti wa awa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi wa iye uja adagwa m'manja a acifwamba?

37. Ndipo anati, iye wakumcitira cifundo. Ndipo Yesu anati kwa iye, Pita, nucite iwe momwemo.

38. Ndipo pakupita paulendo pao iye analowa m'mudzi wina; ndipo mkazi wina dzina lace 4 Marita anamlandira iye kunyumba kwace.

Werengani mutu wathunthu Luka 10